Ulendo wa munthu wanzeru : Nthano ya ophunzira chingerezi
(The Journey of a Wise Man: A Fable for English Learners)
1 Kale-Kale kunali munthu wina wanzeru yemwe amakhala ku dela la m'mapiri. Delali linali lokongola. Koma kunali kovuta kupeza chakudya.
1 A long time ago, there was a wise man living in a mountain country. The country was beautiful. But it was always difficult to find enough food.
2 Anthu a mudera lokwera limeneri anaganiza kuti ayende ulendo pamodzi kupita ku dera lotsika. Nthawi imene matalala adayamba kusungunuka iwo adapachira katundu wawo pa magaleta awo. Mwachiyembekezo komabe mokhumudwa wanzeruyu ndi anansi ake ananyamuka kusiya nyumba zawo ku dera lokwera limeneri.
2 The people of the High Country decided that they would travel together to the Low Country. When the snow began to melt, they packed all they owned into their wagons. With anticipation mixed with sadness, the wise man and his neighbors left their High Country homes.
3 Wanzeruyi anazindikira kuti padali kanthu kena kachilendo komwe kankachitika pomwe adangoyamba ulendo wawo. Akuyenda, tsiku ndi tsiku dzaja lake lakumanja lidayamba kukhala lolimba. Pamene amayenda kuchokera ku dera lokwera limeneri dzanjali limafowokera-fowokera. Zinthu zitatu zidamudabwitsa. Choyamba dzanjali limakhala lofowoka kwambiri akaima m'mudzi. Chachiwiri adawona kuti akakhala pamodzi kuwotha moto usiku ndikumakambirana dzanja lake lamakhalanso lamphamvu.
3 The wise man noticed something strange taking place soon after they began their journey. As they traveled day after day, his right arm began to feel stiff. The further they traveled from the High Country, the weaker it became. Three things puzzled him. First, his arm always felt the weakest whenever they stopped in a village. Secondly, he noticed that when the travelers from the High Country gathered around a fire at night to talk among themselves, his arm became strong again.
4 Chimene adachizindikira kachitatu ndichomwe chidamuzizwitsa kwambiri. Akaika dzanja lake kumbuyo silimakhalanso lolimba komanso lopanda mphamvu.
4 His third discovery puzzled him the most. When he put his arm behind his back, it no longer felt stiff and useless.
5 Tsiku lina munthu wanzeruyu anali odabitsidwa. Ankati akamakhota, pagulaye ali pa galeta lake, adawona kuti ambiri amayika dzanja lawo kumbuyo. Poyang'anitsitsa adawona kuti ena mwa akulu akulu adali atamangirira manja awowo ndi zingwe.
5 One day the wise man was startled. As his wagon rounded a bend in a high mountain road, he looked down on his neighbors' wagons ahead of him. He realized that many others were also holding an arm behind their back. As he looked more closely, he saw that some older people had even tied their arm in place with a rope.
6 Adadabwa kuti kodi zoterozo zinkachitika chifukwa chani?
6 Why, he wondered, was this happening?
7 Potsiliza adafika kudera lotsika. Nyengo idali yofunda. M'Munda mumapezeka chakudya ndipo m'mkhalango mudali mitengo yomangira nyumba. Moyo wawo udali wachiyembekezo. Wachiyembekezo kupatulapo kuti manja awo anali ofowoka. Kunkamveka kuti m'pweya wa mud era lotsika limeneri ndiumene umayambitsa kufooka kwa chilendoko. Ena ankanena kuti adayenerakuti angokuzolowera kufookako ngati angafune kuti akhale m'dera lotsika limeneri.
7 At last they reached the Low Country. The weather was warm. The fields would produce grain and the forests would supply lumber for their houses. Life looked promising. Promising, that is, except for their weak arms. It was rumored that the Low Country's air caused this strange weakness. Some of the people even said they must learn to live with this weakness if they wanted to stay in the Low Country.
8 Akulu ndi ana omwe ankapita kokagwira ntchito. Amagaula m'minda yawo, kubzala mbewu ndi kudala mitengo yomangira nyumba zawo. Telala wa kudera lowerali adasoka bulandi lotsopano loti lizitha kugwirizira dzanja lawolo. Adasokereranso chikopa pa bulandi ndi chilinga choti mapewa awo azintha kukankha katundu wolemera. Ngakhale kuti padali bulandi limeneri, ntchito imachedwebe pachifukwa chakuti aliyense amagwiritsa ntchito dzanja limodzi.
8 The adults and children set to work. They cleared the land, planted crops, and prepared lumber to build their new homes. A High Country tailor sewed a new kind of coat that would hold the useless arm in place. He also put leather on the coat so the shoulder could push heavy loads. Even with the new coat, however, work was slow because everyone used only one arm.
9 Apanso wanzeruyo anatulukira chinthu china chachilendo. Poyamba adawona kuti ngakhale kuti chinali chopweteka kugwiritsa ntchito dzanja lofookalo koma ana adayambanso kugwiritsabe ntchito. Chachiwiri munthu wanzeruyi adazindikiranso kuti panthawi imene anthu a dera lokwerari akakhalira pamodzi m'myumba zapamwamba natseka maitseko zonse ndi mawindo manja awo amakhalanso amphamvu ngakhalenso awokalamba omwe. Ambiri amati izi zikusonyeza kuti m'mpweya wa ku dera lotsikalo udali ndi vuto. Ambiri adavomereza kuti pothetsa vutoli ndibwino kumanga nyumba zolimba kwambiri zoti mpweya wadera lotsikalo usamalowemo. Koma munthu wa nzeruyo anali odabwitsidwa kwambiri powona kuti ana ankawoneka amphamvu kwambiri pamene ankasewera ndi kugwira ntchito panja mu mpweya wadera lotsika limeneli.
9 Again, the wise man noticed a strange thing. First, he noticed that--even though it caused them pain--the children soon began using their weak arm again. Secondly, the wise man noticed that whenever the High Country people met together in their first buildings, if they shut all the doors and windows, strength returned to the arms of even the oldest men and women. "Surely," most said, "this proves that the Low Country air is at fault." Most agreed that the only solution was to build houses so strong that all Low Country air could be kept outside. But the wise man was puzzled most because the children seemed to become stronger while playing and working outside in the Low Country air.
10 Munthu wanzeruyi adali wamantha ndi umoyo wa anthu ake. Bulandi latsopano lidawapangitsa kuti azigwira ntchito mofulumira ndi dzanja limodzi. Koma dzinja lidali litayandikira kotero kuti nyumba zawo ngakhalenso zomera zawo sizikadakhalapo ngati aliyense akadapitirira kugwira ntchito ndi dzanja limodzi.
10 The wise man watched his High Country neighbors trying to build their houses while using only one arm. He became fearful for his people's welfare. The new coat helped them work faster with one arm. But winter was coming and neither the houses nor the crops would be ready if everyone continued to work with one arm behind their back.
11 Munthu wanzeruyo adaphunzirapo kanthu kuchokera kwa ana. Iye adazindikira kuti ngakhale kunali kovuta kugwiritsa ntchito dzanja lofookalo, pogwira ntchito zolimba, komabe yomweyo idali njira yopangira dzanjalo kukhalanso lamphamvu. Popeza kuti chilimwe chidali pafupi adadziwa kuti sanayenera kusiya kugwira ntchito ya nyumba yake kuti alimbitse manja ake. Komanso adadziwa kuti sangatsilize kumanga nyumba yake lisadafike dzinja ngati atakhala kuti sakugwiritsa ntchito manja ake onse. Wanzeruyo adaganiza kuti anayenera kukhala ndi kanthawi tsiku ndi tsiku yoti azilimbitsira manja ake ndichilinga choti atsilize nyumba yake lisadafike dzinja.
11 The wise man learned a lesson from the children. He realized that--even though it was painful--using his weak arm for hard work was the only way to make it strong again. Because winter was coming, he knew that he could not stop working on his house in order to spend all his time trying to make his arm strong. But he also knew that he could not finish his house before winter unless he used both arms. The wise man decided that if he was to finish his house before winter, he must spend some time each day strengthening his arm so that he could finish his house more quickly.
12 Wanzeruyu tsiku ndi tsiku amalimbitsa manja ake komanso kukonza nyumba yake. Adatsiliza nyumba yakeyo dzinja lisanafike.
12 The wise man spent time each day both strengthening his arm and working on his house. He finished his house before winter.
13 Ambiri akudera lokwera limeneri adafa dzinja limenero chifukwa matalala oyala adafika asadakolole mbeu zawo komanso asadatsilize kumanga nyumba zawo. Ankagwira ntchito pong'ono-pang'ono popeza ankawopa kuti akatsiliza nyumba zawo msanga adzasowa chilimbitsira manja awo.
13 Some High Country people perished that winter because the snow came before their crops were harvested and their houses finished. They had worked slowly every day because they were afraid to stop working on their houses long enough to strengthen their weak arm.
14 Ngati mukhala mu United states ndipo simutha kulankhula chingerezi bwino ndiye kuti mukukhala ngati mwanjatilira dzanja lanu limodzi kumbuyo. Muyenera muzigwira ntchito kuti muzisamalira mabanja anu. Koma ngati simukhala ndi nthawi yophunzira chingerezi tsiku ndi tsiku mudzakhala mukuzindikira zochepa moyo wanu wonse. Spoken English Learned Quickly idalembedwa kuti muthe kuphunzira pakhomo komanso ndi kumatha kugwirabe ntchito. Ngati mungamaphunzire chingerezi tsiku liri lonse kwa miyezi isanu ndi umodzi mpakana chaka chingerezi chanu chidzasintha kwambiri. Mudzakhala mukulandira malipiro okwera, kukhala bwino pakati pa anzanu ndi kulankhulana ndi wana wanu pomwe akuphunzira chingerezi msukulu.
14 If you live in the United States and cannot speak English well, you are living as though one arm was tied behind your back. You must work to support your family. But if you do not spend time each day learning English, you will be limited for the rest of your life. Spoken English Learned Quickly was written so that you can study at home and still hold a job. If you will regularly study English each day for six months to a year, your English will greatly improve. You will be more able to earn higher wages, live more effectively in your community, and talk with your children as they learn English in school.
Spoken English Learned Quickly | The Journey of a Wise Man |
| Copyright 2004 Spoken Language International (www.FreeEnglishNow.com): The Journey of a Wise Man may be reproduced without written permission provided that it is unaltered and carries this copyright notice in full with the web site address. It may be reproduced in either one or both languages. |